News, Radio Alinafe

AMBUYE TAMBALA APEMPHA ZIPANI ZAMUMPINGO KUFIKIRA ACHINYAMATA KU MAPARISHI AWO

Ambuye George Desmond Tambala, Arkiepiskopi wa Arkidayosizi yaKatolika ya Lilongwe, apempha zipani za ansembe komanso ma sisitele mu arkidayosiziyi kuti afikire achinyamata m’maparishi osiyanasiyana ndi cholinga choti azimvetsesa nkhani za mayitanidwe.
Ambuye Tambala ayankhula izi la Mulungu la Mayitanidwe, 21 April 2024 ku Parishi ya Mlare pa mwambo wa nsembe ya misa yomwe achinyamata mu Arkidayosiziyi amakondwelera tsikuli.
Malingana ndi Ambuye Tambala, achinyamata amasowa ansembe komanso ma sisitele kuti adziwaunikira pa nkhani ya mayitanidwe.
“Ndawapempha ansembe komanso ma sisitele mu arkidayosizi yathu, kuti tsiku la mayitanidwe lisathere pomwepa koma akuyenera kumawayendelabe achinyamatawa ku maparishi awo ndikuwaphunzitsa zosiyanasiyana zokhudza zipani zawo chifukwa achinyamatawa akumawasowa kwambiri, choncho ndawapempha kuti zisathere pomwepa ayi,” anatero ambuye Tambala.
Ambuye George Desmond Tambala, Arkiepiskopi wa Arkidayosizi yaKatolika ya Lilongwe
Ambuye Tambala atinso kudzera ku Arkidayosiziyi akhazikitsa gulu lomwe lidziliimbikitsa achinyamata m’magawo osiyanasiyana pa moyo wawo.
Gululi lili ndi anthu osiyanasiyana kuphatikizapo m’modzi wa akatswiri pankhani yoyimba a Ben Micheal komanso mphunzitsi wakale wa timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino, a Young Chimodzi.
Ndipo mkulu owona za Mayitanidwe mu Arkidayosizi ya Lilongwe, bambo Kelvin Khodola apempha achinyamata kumvetsera mozama komanso kumalingalira za mayitanidwe awo.
Mmawu ake, wapampando wabungwe la achinyamata mu Arkidayosizi ya Lilongwe, Chisomo Nkhoma wayamikira pempho lomwe ambuye George Desmond Tambala apeleka, ponena kuti zithandiza achinyamatawa kumakhala ndi zisankho zabwino pankhani ya mayitanidwe akamakumana ndi ansembe komanso ma sisitele m’ma Parish awo.
Chisomo Nkhoma, wapampando wabungwe la achinyamata mu Arkidayosizi ya Lilongwe
Mwambo wansembe yamisa yokondwelera chaka chamayitanidwe unatsogolera ndi Ambuye mthandizi a Arkidayosizi ya Lilongwe, ambuye Vincent Mwakhwawa.
Mutu wa mayitanidwe chaka chino ndiwoti “Achinyamata pamene mukuyitanidwa kudzala mbeu za chiyembekezo ndi kumanga mtendere, pitani mukayitane aliyense kuti abwere kuphwando.”
Wolemba ndi Titus Jata Phiri