News

BUNGWE LA CAT LILIMBIKITSA ULIMI WA MAWUNGU AKULUAKULU (GIANT PUMPKINS)

Bungwe la Centre for Agricultural Transformation (CAT) lapempha alimi m’dziko muno kuyamba kubzala mbeu ya maungu akuluakulu (Giant Pumpkins) ndi cholinga chofuna kuchepetsa njala yomwe imakuta dziko lino chaka ndi chaka.

Izi zayankhulidwa lachisanu pa 16 February 2024 pamwambo wachionetsero cha mbewu ya mawunguyi, yomwe ikutchedwa NRC Giant Pumpkin, yomwe inalimidwa miyezi ingapo yapitayi ku munda wachitsanzo wabungweli ku NRC m’boma la Lilongwe.

M’modzi mwa akuluakulu a bungwe la CAT, Mayi Lizzie Kachulu ati mawunguwa athandiza alimi kukhala odzidalira pa chakudya komanso chuma.

Iwo ati kucha msanga kwa mbewuyi ndikothandiza anthu ambiri maka m’miyezi yomwe njala imavuta ya Janyuwale komanso February.

“Mawungu amenewa ndi osiyana ndi amene alimi amabzala, awawa ali ndi dzina loti Giant Pumpkins (Mawungu akuluakulu). Alimi akakhala kuti asamala bwino, ayika manyowa okwanira amalemera kuyambira ma kilogalamu atatu mpaka 30. Ndipo chimene timafuna kuti alimi adzaone ndi choti atati alimi apatsidwa mbeu iyiyi, mabanja awo atha kukapindula,” anatero a Kachulu.

Mayi Lizzie Kachulu, Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe la CAT

 

M’mawu ake, m’modzi mwa akadaulo pankhani za ulimi ku sukulu ya ukachenjede ya NRC, Shaibu Kananji ati mbewuyi ili ndi kuthekera kothandiza alimi kupeza phindu lochuluka pa ulimi wawo.

Iwo anatsindikanso kunena kuti mbewuyi sinapangidwe kuti idzalowe mmalo mwa mbewu ya mawungu yomwe ilipo kale koma kuti ithandize alimi kukhala ndi chakudya chokwanira.

“Cholinga kwenikweni ndi chonena kuti, chifukwa choti mawungu awawa amabereka mwansanga ndi ambiri (akuluakulu komanso olemera), mlimi atha kupindula kwambiri. Mlimi atha kusankha kuti akabzale mawungu a local aja mmene amadzalira, koma awawa akabzaleso pamalo pomwe sipafuna pakhaleso chimanga ayi,” anatero a Kananji.

Shaibu Kananji, mmodzi mwa akadaulo pankhani za ulimi ku sukulu ya ukachenjede ya NRC

Poyankhulapo pambuyo pachiwonetselochi, mfumu yaikulu Mazilo 2 yayamikira mbewuyi ponena kuti iwombola anthu ochuluka omwe amakumana ndi njala chaka ndi chaka.

“Mawungu amenewa ndi osiyana ndi amene timakumana nawo makukamu (ana akwanire), awawa ndi mawungu oti nyumba anthu akaphika kaya muli anthu 10, dzungu limodzi litha kuwaombola onsewo,” anamaliza motero a mfumu Mazilo 2.

Mfumu yaikulu Mazilo 2, imodzi mwa mafumu omwe anali nawo pachionetsero cha mawungu akuluakulu

Bungwe la CAT likugwira ntchito ndi magulu osiyanasiyana pantchito yopititsa patsogolo ulimi pogwilitsa ntchito njira zamakono pofuna kuti mzika za dziko lino zisiye kudalira mtundu umodzi wa mbewu.

 

 

Wolemba: Eric Norman Mkwaira