Amayi abungwe la CWA mu Arkidayosizi ya Lilongwe, awalimbikitsa kukhala ogwirizana ndicholinga chopititsa mpingo wakatolika patsogolo pankhani za chitukuko komanso chikhulupiriro chawo.

Izi zayankhulidwa ndi Bambo Augustine Katundu omwe ndi bambo mlangizi wa bungwe la amayi mu arkidayosizi ya Lilongwe, loweluka pa mwambo wokondwerera unakubala mu mpingo wa Katolika ku Maula podium, omwe anautchula kuti Chilundu Gala.

Bambo Katundu apempha amayi kukhala odzidalira maka posamalira mabanja awo komanso kutumikira mpingo modzipereka potengera chitsanzo cha momwe amayi Maria amachitira.
Wapampando wabungwe la CWA, mu arkidayosizi ya Lilongwe, a Louiser Kamwaza, ati amayi ali ndi udindo osamalira mabanja, ana awo komanso kutumikira mumpingo ponena kuti amayi ndiye tsinde la mpingo.
A Kamwaza ati mkunowu, wathandizira kupeza ndalama zomwe zithandizire bungwe lawo kupita chitsogolo pankhani za chitukuko mumpingo wakatolika komanso kuthandizira kuchita ntchito za chifundo.
Pa mwambowu, bungweri la CWA, linakonza latundu osiyanasiyana amene anagulitsidwa kuphatikizapo Raffle draw yomwe amayi ena anapata mphoto yowina katundu monga chipangizo cha makono chophikira, Mattress komanso thumba la feteleza lolemera makilogram 50.
Wolemba ndi Mercy Lwanja

