News

CHIPANI CHA A SISTERE CHA M.M.M CHAYAMIKILIDWA KAMBA KA NTCHITO ZAKE MU ARKIDAYOSIZI YAKATOLIKA YA LILONGWE

Wolemba ndi Sam Kalimba
Arkidayosizi ya Lilongwe yayamikira ndi kulimbikitsa a sistere a chipani cha Missionaries of Mary Mediatrix (M.M.M) kamba ka utumiki wawo womwe ati akuwugwira modziyiwala mu Arkidayosiziyi.
Arkiepisikopi wa Arkidayosiziyi George Desmond Tambala ndiwo ayankhula izi pa mbuyo pa mwambo wa Misa ya malumbiro oyamba a Sr. Apronia Mahowe ndi Sr. Stella Mkwezalamba a chipanichi ku parish ya Kaggwa Loweruka pa 27 January 2024.
Ambuye Tambala anati iwo akudziwa bwino m’mene amayi achipanichi akugwirira ntchito zothandiza anthu pachipatala cha Mlare.
M’mau ake, bambo mfumu wa parish ya Andrea Kaggwa Woyera Monsignor Patrick Thawale wayamikira ntchito zomwe amayiwa akugwira pa parishiyi monga kuphunzitsa ana pa sukulu ya Wisdom Center komanso kuthandizira pa misa za ku ma outstation.
Mayi mkulu wa chipani cha Missionaries of Mary Mediatrix Sr. Mercedes Arbesu ochokera ku likulu la chipanichi ku Spain anali nawo pa mwambowu.