News

ACHINYAMATA OKWANA 97 ALANDIRA SAKRAMENTI LA ULIMBITSO PA PARISH YA ST PATRICKS MU ARKIDAYOSIZI YA LILONGWE

Dean wa Mtima Woyera Deanery, Bambo Augustine Katundu ati sakramenti la ulimbitso likuyenera kukhala lothandiza achinyamata amene alandira ulimbitso pakutumikira mulungu tsiku ndi tsiku.
Bambo Katundu ayankhula izi Loweruka pa 02 September 2023 pambuyo pa mwambo wa sakramenti la ulimbitso omwe achinyamata okwana 97 alandira pa Parish ya St Patricks, mu Arkidayosizi ya Lilongwe.
Bambo Augustine Katundu kugawa ulariki wawo
Bambo Katundu ati “ulimbitso simathero a zonse” maka pomwe achinyamata ena amapezeka akusiya kutumikira mu mpingo.
Iwo apempha achinyamatawa kuti alowe nawo m’magulu osiyanasiyana opezeka mu mpingo omwe ndikuphatikizapo a Legio, makwaya komanso a achinyamata mwa ena.
Mmodzi mwa akuluakulu pa parishiyi, a Vincent Nkhoma apempha akhristu kuti azilimbikitsa ana awo kupita kumaphunziro osiyanasiyana a ma sakramenti ndi cholinga chofuna kukhala ndi akhristu othandiza mpingo pofalitsa mawu a mulungu.
Iwo ati “tialimbikitse makolo komanso achinyamata kuti awone ubwino omalizitsa chinamwali chimenechi cha mpingo chimene chimayamba ndi ubatizo.”
Ndipo mmodzi mwa ana omwe alimbitsidwa kuchokera ku outstation ya Kauma, Maria Richard Mwenyedada walimbikitsa anzake kuti akalimbitsidwe popita ku maphunziro monga a Tilotonse mwa ena.
Wolemba: Eric Norman Mkwaira