News

AMBUYE TAMBALA ALIMBIKITSA AKHRISTU APA PARISH YA BANJA LOYERA KUKONDA MOYO OPEMPHERA

Arki-episkopi George Desmond Tambala wa Arkidayosizi ya Lilongwe, wapempha akhristu apa Parish ya Banja Loyera (Chilinde) kuti akuyenera kukhala olimbika pa moyo wawo wa uzimu, kudzera m’kupemphera nthawi zonse.

Ambuye Tambala apeleka pempholi loweluka pa 28 December 2024, pa mwambo wa nsembe ya Misa yokondwerera kuti Parish’yi, yakwanisa za 50 chiikhazikitsileni (Golden Jubilee).

Malingana ndi Ambuye Tambala, ngati akhristu akhale ozama pa moyo wa uzimu, zithandiza kwambiri kutukula mpingo m’magawo osiyanasiyana.

Ambuye Tambala ayamikiranso akhristu apa Parishiyi kamba ka m’gwirizano omwe ulipo komanso zitukuko zosiyanasiyana zomwe zikuchitika.

“Pa zaka 50 zimenezi taona ndithu kukula kwa mpingo, kukula kwa moyo wa akhristu eni ake komanso mabanja, nde ndikufuna ndiwalimbikitse kuti apitilize kumanga moyo wawo wachikhristu. Komanso tiwayayimikire ngati Parish kuti akuchita zikutuko zosiyanasiyana monga tawonera kuti akumanga nyumba ya ansembe, zomwe zikuonesa kuti akhristu akuno akugwirizana”

Powonjezera, Ambuye Tambala ati ngati Arkidayosizi pali chinkonzero choti chaka cha mawa (2025), ayambe kupeleka msulo ku mabanja achikatolika mu Arkidayosiziyi, ndicholinga chofuna kukhala ndi ma banja olimba mu mpingo.

“Ndondomekoyi iripo koma idzalengezedwa bwino munthawi yake ndipo iyambika posachedwapa”

M’mawu ake, wachiwiri kwa wapampando wa Parish ya Banja Loyera a Wirald Njikho, anati ndiwokondwa kuti Parishiyi yakwanisa zaka 50, ponena kuti wakhala ulendo wautali kuti afike pomwe ali pano.

A Njikho atiso ngati Parish, agwiritsa ntchito pempho lomwe Ambuye Arki-episkopi George Desmond Tambala apeleka pankhani yolimbikitsa moyo wachikondi, komanso kulimbikitsa moyo wa uzimu pakati pa akhristu.

Pa chakachi panaliso kupeleka ma satifiketi kwa ansembe ena omwe anatumikirapo pa Parishiyi, komanso mabanja omwe akhala zaka zambiri akadali pabanja, ndi atsogoleri ena omwe agwira ntchito yotamandika pa Parishiyi.

Parish ya Banja Loyera (Chilinde), idatsegulidwa mchaka cha 1974, ndipo ma Parish a Utatu woyera (Kawale), Don Bosco (Area 23), St Mary’s (Kamuzu Barracks) ndi St Philip (Area 44), ndima Parish omwe abadwa kuchokera mu Parish ya Banja Loyera.