“Achinyamata Asinkhesinkhe za Mayitanidwa Awo; Lero osati mawa,” Ambuye George Tambala
Achinyamata mu Arkidayosizi ya Lilongwe, apemphedwa kuti akuyenera kugwiritsa ntchito mwayi komanso kupanga ziganizo zoyenera pa momwe angatumikire Mulungu kudzera mmayitanidwe awo.
Ambuye George Desmond Tambala a Arkidayosizi ya Lilongwe, ndiomwe apeleka pempholi lero pa 09 March 2025 ku Parish ya St. Mathias (Lumbadzi) pa mwambo wa nsembe ya Misa yotsekulira zochitikachitika za tsiku la Mulungu la mayitanidwe Mpingo (Vocation Sunday).

Ambuye Tambala ati uwu ndimwayi oti achinyamata asinkhesinkhe ndikumva komanso kusankha mayitanidwe omwe Mulungu akuwayitanira, kuti atumikile mpingo waKatolika.
“Pempho langa kwa achinyamata ndiloti asinkhesinkhe za kuyitanidwa kwawo , komanso asankhe osakhala mawa, koma lero, chifukwa achinyamata ambiri amazinamiza kuti ndizasankha mawa pankhani yamayitanidwe awo,” anatero ambuye Tambala.
Mkulu owona za mabungwe a utumiki wa Papa (PMS) mu Arkidayosizi ya Lilongwe, bambo Geoffrey Chikapa, ati ofesi yawo ikhala ikupereka maphunzitso osiyanasiyana kwa achinyamata, ndi cholinga choti athe kumvetsa bwino pankhani ya mayitanidwe pa moyo wawo wachikhristu.
“Ngati ofesi yowona za mabungwe a utumiki wa Papa, tigwira ntchito molumikizana ndi bungwe lomwe limaona za achinyamata, komanso gulu lomwe limayang’anira zamayitanidwe mu Arkidayosizi yathu, tikhala tikuyendera achinyamata kuwalimbikitsa komanso kupereka mauthenga osiyanasiyana okhudzana ndi mayitanidwe.”

Ndipo m’mawu awo, Sister Agness Mwamba achipani cha Franciscan Missionary Sisters of Asis, omweso ndi mlembi ku gulu loyang’anira zamayitanidwe mu Arkidayosizi ya Lilongwe, ati athandizira kupereka maphunzitso osiyanasiyana kwa achinyamata m’maparishi, kuti athe kumvetsa bwino zamayitanidwe pa moyo wawo.
Mutu wa chaka chino wa la Mulungu la mayitanidwe mu Mpingo ndi “Achinyamata Ndi Atumiki Achiyembekezo,” ndipo chakachi chidzachitika pa 10 May 2025.
Wolemba ndi Titus Jata Phiri